• +265 999 311 641
  • info@csatmw.org
  • Lilongwe Area 49, Opposite Best Oil Chinese Complex
Articles
Musabe ndalama za kolera-CSAT

Musabe ndalama za kolera-CSAT

Bungwe lothandizira ulamuliro wa bwino m’dziko la Center for Social Accountability and Transparency (CSAT) lachenjeza ma ofesala ogwira ntchito m’boma komaso mabungwe omwe siaboma kuti apewe mchitidwe wa katangale komaso kuzembetsa katundu yemwe akugwiritsidwa ntchito pa nkhondo yolimbana ndi matenda a kolera.

Izi adalankhula ndi mkulu wa bungwe la CSAT a Willy Kambwandira la chitatu sabata ino mu mzinda wa Lilongwe pamene bungwe lawo limawulutsa ndondomeko zina zomwe a Malawi akhoza kutsata kuti apereke nkhawa zawo kapene kuneneza mchitidwe wa katangale pa nambala yawo ya ulere ya 3056.

A Kambwandira adafotokoza kuti tsopano a Malawi akhozaso kupereka nkhawa zawo kapena kuneneza mchitidwe wa katangale omwe anthu ena akuchita pa ntchito yolimbana ndi Ngozi zogwa mwadzidzi kuphatikizako matenda a kolera.

“Ndi zochititsa manyazi kwambiri kuti anthu ena adangobadwa ndi mtima oipa wakuba. Kotero alibe chisoni amatengelapo mwayi pachina chilichonse kuphatikizako Ngozi zogwa madzidzi komaso matenga ngati kolera kuti abe ndalama kapena kuzembetsa katundu yemwe cholinga chake ndikuthandiza nathu ovutikitsitsa komaso osauku.

Ndiye tikuna kuchenjeza ma ofesala onse omwe akugwira ntchito yolimbana ndi matenda a kolera kuti apewe mchitidwe wa katangale. Tikuwachejeza kuti asabe ndalama komaso zipangizo zolimbimanirana ndi matendawa,” adatero a Kambwandira.

Iwo adowonjezera kunena kuti dziko la Malawi likulephera kutukuka kaamba ka mchitidwe wa katangale komaso kupondelezedwa kwa anthu osauka. Kotero amema a Malawi kuti azineneza anthu onse amene akuchita mchitidwe wa kakatangale pa ncthito za chitukuko poimba nambala ya bungwe la CSAT 3056 mwaulere.

A Kambwandira adafotokoza motere: “Choyambilira chimene anthu akuyenera kuchita asadaimbe nambala ya ulelereyi ndikufunsa kapena kuneneza za katangale kwa a dindo akudera kwawo monga a khansala ndi makomiti a zachitukuko. Ndipo ngati sakukhutira akatsata njira zonsezi, akhoza kutiyimbira ife a CSAT pa nambala ya ulere ya 3056.”

Polankhulapo pa mlili wa Kolera omwe wapha anthu pafupifupi 881 chiyambileni, a Kambwandira adati izi zadza kaamba kakulephwera kutumikira bwino anthu maka-kaka opezeka m’madera akumudzi.

“Sizoona kuti tsiku la lero a Malawi azimwa madzi opezeka m’malo onyasa ngati mzithamphwi chonsecho boma limapereka ndalama zankhani nkhani kuti a phungu ndi nthambi zina za boma zizingwira ncthito za chitukuko kuti miyoyo ya anthu ipite pa tsogolo m’dziko muno. Tikunena pano, dziko la Malawi lakwanitsa zaka 56 lili pa ufulu odzilamulira lokha. Koma chonsecho anthu ambiri m’dera akumidzi ndi mjigo omwe wa madzi sawudziwa kuti umaoneka bwanji. Izi ndizomvetsa chisoni kwambiri. Chiyambilira ngati dziko tikuyenera kusamalira miyoyo ya anthu ngati kuwapatsa madzi awukhondo chifukwa anthuwa ndi amene amtiika m’maudindo osiyana siyana,” adatero a Kambwandira.

Pakadali pano bungwe la CSAT likugwira ntchito ndi mabungwe ena komaso nthambi zina za boma ngati bungwe la Anti-Corruption Bureau (ACB) pa ncthito yofufuza komaso kutsekula milandu ya katangale m’dziko muno.